35 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye.” Choncho chiwandacho chinagwetsa munthuyo pansi pakati pawo, kenako chinatuluka mwa iye osamuvulaza.+
38 Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, kuti Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye,+ anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.+