23 Tsopano asilikaliwo atamupachika Yesu, anatenga malaya ake akunja ndi kuwagawa m’zigawo zinayi, kuti msilikali aliyense atenge chigawo chimodzi. Panalinso malaya amkati. Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anali owombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi.+