Machitidwe 11:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Mmodzi wa iwo dzina lake Agabo,+ analosera mwa mzimu kuti padziko lonse lapansi kumene kuli anthu,+ padzagwa njala yaikulu. Izi zinachitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo. Machitidwe 16:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kenako iwo anapita ku Fulugiya ndiponso m’dziko la Galatiya,+ chifukwa mzimu woyera unawaletsa kulankhula mawu opatulika m’chigawo cha Asia. Machitidwe 21:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Iye anafika kwa ife ndi kutenga lamba wa Paulo. Kenako anadzimanga mapazi ndi manja ndi kunena kuti: “Mzimu woyera wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga+ chonchi ku Yerusalemu ndi kumupereka+ m’manja mwa anthu a mitundu ina.’” 1 Timoteyo 4:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Komabe, mawu ouziridwa amanenadi kuti m’nthawi zam’tsogolo,+ ena adzagwa+ pa chikhulupiriro, chifukwa chomvetsera mawu ouziridwa omwe ndi osocheretsa,+ ndiponso ziphunzitso za ziwanda.+
28 Mmodzi wa iwo dzina lake Agabo,+ analosera mwa mzimu kuti padziko lonse lapansi kumene kuli anthu,+ padzagwa njala yaikulu. Izi zinachitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo.
6 Kenako iwo anapita ku Fulugiya ndiponso m’dziko la Galatiya,+ chifukwa mzimu woyera unawaletsa kulankhula mawu opatulika m’chigawo cha Asia.
11 Iye anafika kwa ife ndi kutenga lamba wa Paulo. Kenako anadzimanga mapazi ndi manja ndi kunena kuti: “Mzimu woyera wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga+ chonchi ku Yerusalemu ndi kumupereka+ m’manja mwa anthu a mitundu ina.’”
4 Komabe, mawu ouziridwa amanenadi kuti m’nthawi zam’tsogolo,+ ena adzagwa+ pa chikhulupiriro, chifukwa chomvetsera mawu ouziridwa omwe ndi osocheretsa,+ ndiponso ziphunzitso za ziwanda.+