13 Pamenepo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anapitiriza kuyenda mumsewu. Simeyi anali kuyenda m’mbali mwa phiri pafupi ndi Davide ndipo anali kuyenda akulankhula mawu onyoza.+ Iye analinso kuponya miyala akuyenda m’mbali mwa phirimo pafupi ndi Davide ndiponso anali kuwaza fumbi lambiri.+