-
Machitidwe 14:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 kuti: “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu+ okhala ndi zofooka+ ngati inu nomwe, ndipo tikulengeza uthenga wabwino kwa inu. Tikuchita izi kuti musiye zachabechabe zimenezi+ ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo,+ amene anapanga kumwamba,+ dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.
-
-
Chivumbulutso 19:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pamenepo ndinagwada pansi n’kuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire.+ Koma iye anandiuza kuti:+ “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+ Lambira Mulungu,+ pakuti kuchitira umboni za Yesu ndiko cholinga cha maulosi.”+
-