7 Mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova anaimirira+ chapafupi, ndipo kuwala kunaunika m’chipinda cha ndendecho. Kenako mngeloyo anadzutsa Petulo mwa kumugunda m’nthiti,+ n’kunena kuti: “Dzuka msanga!” Pamenepo maunyolo amene anamumanga nawo manjawo anagwa pansi.+