19 Herode+ anafunafuna Petulo pena paliponse, ndipo atalephera kumupeza, anapanikiza alondawo ndi mafunso ndi kulamula kuti awatenge, akawapatse chilango.+ Pamenepo Herode anachoka ku Yudeya ndi kupita ku Kaisareya, kumene anakhalako kanthawi ndithu.