25 Inu ndinu ana+ a aneneri ndi a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo anu akale. Iye anauza Abulahamu kuti, ‘Kudzera mwa mbewu yako mabanja onse a padziko lapansi adzadalitsidwa.’+
8 “Anamupatsanso pangano la mdulidwe.+ Chotero anabereka Isaki+ ndi kuchita mdulidwe wake tsiku la 8.+ Isaki naye anabereka Yakobo, Yakobo anabereka mitu ya mabanja 12 ija.+