26 Tsopano mukuona ndipo mukumva za Paulo ameneyu, kuti si mu Efeso+ mokha muno mmene wakopa anthu ambirimbiri ndi kuwapatutsira ku chikhulupiriro china. Wachita zimenezi pafupifupi m’chigawo chonse cha Asia. Iye akumanena kuti milungu yopangidwa ndi manja+ si milungu ayi.