18 Pakuti anthu oterowo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a mimba zawo.+ Ndipo mwa kulankhula mawu okopa+ ndi achinyengo+ amanyenga anthu oona mtima.
14 Ali ndi maso odzaza ndi chigololo+ komanso olephera kupewa kuchita tchimo,+ ndipo amakopa anthu apendapenda. Ali ndi mtima wophunzitsidwa kusirira mwansanje.+ Iwo ndi ana otembereredwa.+