39 Pamenepo Petulo ananyamuka n’kupita nawo limodzi. Atafika kumeneko, iwo anamutengera m’chipinda cham’mwamba chija. Ndipo akazi onse amasiye anabwera kwa iye akulira ndi kumuonetsa malaya ambiri akunja ndi amkati+ amene Dorika anali kusoka pamene anali nawo.+