-
Aroma 6:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Ndikulankhulatu monga munthu chifukwa cha kufooka kwa matupi anu.+ Pakuti mmene munaperekera ziwalo zanu+ kuti zikhale akapolo a zonyansa+ ndiponso akapolo a kusamvera malamulo ndi cholinga chakuti muzichita zinthu zophwanya malamulo, perekaninso ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a chilungamo kuti muzichita ntchito za chiyero.+
-