1 Atesalonika
4 Pomalizira abale, tinakulangizani za mmene muyenera kuyendera+ ndi mmene muyenera kukondweretsera Mulungu, ndipo mukuchitadi zimenezo. Tsopano tikufuna kukudandaulirani ndi kukupemphani m’dzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi mowonjezereka.+ 2 Pakuti mukudziwa malamulo+ amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.
3 Mulungu akufuna kuti mukhale oyera+ mwa kupewa dama.*+ 4 Akufunanso kuti aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake+ m’njira yoyera+ kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, 5 osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana,+ ngati chimene anthu a mitundu ina+ osadziwa Mulungu+ ali nacho. 6 Koma akufuna kuti pasapezeke wina wopweteka m’bale wake kapena womuphwanyira ufulu wake pa nkhani imeneyi,+ chifukwa Yehova adzalanga anthu onse ochita zimenezi,+ monga mmene tinakuuzirani kale ndi kukufotokozerani momveka bwino.+ 7 Pakuti Mulungu sanatiitane mwa kulekerera zodetsa, koma kuti tikhale oyera.+ 8 Choncho munthu wonyalanyaza+ chiphunzitso chimenechi sakunyalanyaza munthu, koma Mulungu+ amene amaika mzimu wake woyera+ mwa inu.
9 Koma za kukonda abale,+ n’zosafunika kuti tizichita kukulemberani pakuti inu nomwe, Mulungu amakuphunzitsani+ kukondana.+ 10 Ndipo inu mukuchitadi zimenezi kwa abale onse ku Makedoniya konse. Koma tikukudandaulirani abale kuti mupitirize kutero mowonjezereka. 11 Ndiponso muyesetse kukhala mwamtendere,+ kusalowerera mu nkhani za eni,+ ndi kugwira ntchito ndi manja anu+ monga mmene tinakulamulirani. 12 Mutero kuti muziyenda moyenerera+ pamaso pa anthu akunja*+ ndiponso kuti mukhale osasowa kanthu.+
13 Komanso abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za amene akugona+ mu imfa, kuti musachite chisoni mofanana ndi mmene onse opanda chiyembekezo+ amachitira. 14 Pakuti ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa ndi kuukanso,+ ndiye kuti amenenso agona mu imfa kudzera mwa Yesu, Mulungu adzawasonkhanitsa kuti akhale naye limodzi.+ 15 Pakuti tikukuuzani izi mogwirizana ndi mawu a Yehova+ kuti, ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye,+ sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. 16 Chifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba,+ ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo,+ ndi lipenga+ la Mulungu. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba.+ 17 Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo,+ tidzatengedwa+ m’mitambo+ kukakumana+ ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.+ 18 Choncho, muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.