1 Atesalonika
3 Choncho pamene sitinathenso kupirira, tinaona kuti ndi bwino tingotsala tokha ku Atene.+ 2 Chotero tinatumiza Timoteyo+ m’bale wathu ndi mtumiki wa Mulungu pa uthenga wabwino+ wonena za Khristu, kuti adzakulimbitseni ndi kukutonthozani pa chikhulupiriro chanu, 3 kuti pasapezeke wina wopatutsidwa ndi masautso+ amenewa. Pakuti inu nomwenso mukudziwa kuti tinayeneradi kukumana ndi zimenezi.+ 4 Ndiponso pamene tinali nanu limodzi, tinali kukuuziranitu+ kuti tiyenera kudzakumana ndi masautso,+ ndipo mmene zachitikiramu ndi mmenenso inu mukudziwira.+ 5 Ndiye chifukwa chake pamene sindinathenso kupirira, ndinamutuma kuti ndidziwe za kukhulupirika+ kwanu, kuti mwina mwa njira ina, Woyesayo+ angakhale atakuyesani, ndipo ntchito imene tinagwira mwakhama ingakhale itapita pachabe.+
6 Koma Timoteyo wangofika kumene kwa ife kuchokera kwa inu+ ndipo watiuza nkhani yabwino ya kukhulupirika kwanu ndi chikondi+ chanu. Akuti mukupitiriza kutikumbukira nthawi zonse, ndiponso mukulakalaka kutiona, monganso mmene ife tikulakalakiradi kukuonani.+ 7 Ndiye chifukwa chake abale, mwa kukhulupirika kumene mukusonyeza,+ mwatilimbikitsa+ m’kusowa kwathu konse ndi m’masautso athu onse. 8 Ndipo ife tsopano tilidi ndi moyo chifukwa inu mukukhala olimba mwa Ambuye.+ 9 Kodi Mulungu tingamuyamike bwanji pa nkhani ya inuyo, kuti timubwezere chifukwa cha chimwemwe+ chonse chimene tili nacho chifukwa cha inuyo pamaso pa Mulungu wathu? 10 Komanso usiku ndi usana timapereka mapembedzero amphamvu+ kuti tidzaone nkhope zanu ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.+
11 Tsopano Mulungu wathu ndi Atate mwiniyo, ndi Ambuye wathu Yesu,+ atitsogolere pa ulendo wathu wobwera kwa inu kuti zonse ziyende bwino. 12 Komanso, Ambuye akuthandizeni kuti muwonjezereke,+ ndiponso kuti chikondi+ chanu kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse chikule. 13 Achite zimenezi mpaka atalimbitsa mitima yanu ndi kukupangitsani kukhala opanda cholakwa+ ndi oyera pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate, pa nthawi ya kukhalapo*+ kwa Ambuye wathu Yesu, limodzi ndi oyera ake onse.+