Kodi Mukulondola Khalidwe Labwino?
“Ngati kuli chokoma mtima [“chabwino,” NW] china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”—AFILIPI 4:8.
1. Kodi khalidwe loipa nchiyani, ndipo nchifukwa ninji silinaipse kulambira kwa Yehova?
KHALIDWE loipa ndilo khalidwe lowonongeka kapena lopotoka. Ilo lili ponseponse m’dziko limene tikukhalamoli. (Aefeso 2:1-3) Komabe, Yehova Mulungu sadzalola kulambira kwake koyera kuipsidwa. Zofalitsa zachikristu, misonkhano yampingo, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo zimatipatsa machenjezo apanthaŵi yake ponena za khalidwe losalungama. Timalandira thandizo labwino la m’Malemba kuti ‘tigwirizane nacho chabwino’ pamaso pa Mulungu. (Aroma 12:9) Choncho, monga gulu, Mboni za Yehova zikuyesetsa kukhala zoyera, zakhalidwe labwino. Koma bwanji za ife aliyense payekha? Ee, kodi inuyo mukulondola khalidwe labwino?
2. Kodi khalidwe labwino nchiyani, ndipo nchifukwa ninji kukhalabe ndi khalidwe labwino kumafuna kuyesayesa?
2 Khalidwe labwino ndilo ukoma, ubwino, machitidwe ndi malingaliro olondola. Si mkhalidwe wosachita kanthu, koma wa zochita zambiri ndi wothandiza. Khalidwe labwino sindilo kungopeŵa uchimo basi; limatanthauza kulondola chabwino. (1 Timoteo 6:11) Mtumwi Petro analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Muwonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu.” Motani? Mwa ‘kutengeraponso [pamalonjezo a mtengo wapatali a Mulungu] changu chonse.’ (2 Petro 1:5) Chifukwa cha mkhalidwe wathu wauchimo, pamafunika kuyesetsadi kuti tikhalebe ndi khalidwe labwino. Komabe, anthu oopa Mulungu akale anachita zimenezo, ngakhale atayang’anizana ndi zopinga zazikulu kwambiri.
Analondola Khalidwe Labwino
3. Kodi Mfumu Ahazi anali ndi mlandu wa zoipa zotani?
3 Malemba ali ndi nkhani zambiri za awo amene analondola khalidwe labwino. Mwachitsanzo, lingalirani za Hezekiya wa khalidwe labwinoyo. Atate wake, Ahazi Mfumu ya Yuda, mwachionekere ankalambira Moleki. “Ahazi anali wazaka makumi aŵiri poloŵa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi m’Yerusalemu; koma sanachita zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake; popeza anayenda m’njira ya mafumu a Israyeli, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli. Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.” (2 Mafumu 16:2-4) Ena amati ‘kupititsa pamoto’ kunali ngati mwambo woyeretsa ndipo osati kupereka munthu nsembe. Komabe, buku lakuti Molech—A God of Human Sacrifice in the Old Testament, lolembedwa ndi John Day, likuti: “Zinthu zina zakale ndi za Punic [Carthaginian] zili ndi umboni, limodzinso ndi umboni wa zofukulidwa m’mabwinja, kuti Akanani . . . anali kupereka anthu nsembe, chotero palibe chifukwa chokayikirira zonena za Chipangano Chakale [za kupereka anthu nsembe].” Ndiponso, 2 Mbiri 28:3 imanena molunjika kuti Ahazi ‘anapsereza ana ake m’moto.’ (Yerekezerani ndi Deuteronomo 12:31; Salmo 106:37, 38.) Kuipatu nanga zochita zake!
4. Kodi Hezekiya anachita motani pakati pa anthu akhalidwe loipa okhaokha?
4 Kodi zinamkhalira bwanji Hezekiya pakati pa anthu akhalidwe loipa okhaokha ameneŵa? Salmo la 119 nlosangalatsa, popeza ena amakhulupirira kuti Hezekiya ndiye analilemba, ndipotu akali kalonga. (Salmo 119:46, 99, 100) Choncho mikhalidwe yake ikusonyezedwa ndi mawu akuti: “Nduna zomwe zinakhala zondineneza; koma mtumiki wanu analingirira malemba anu. Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni.” (Salmo 119:23, 28) Pokhala atazingidwa ndi ochita chipembedzo chonyenga, a m’nyumba ya mfumu ayenera kuti ankamnyodola Hezekiya, kwakuti anavutika kupeza tulo. Komabe, analondola khalidwe labwino, m’kupita kwa nthaŵi anakhala mfumu, “nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova . . . Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israyeli.”—2 Mafumu 18:1-5.
Anasungabe Khalidwe Labwino
5. Kodi Danieli ndi anzake atatu anayang’anizana ndi mayesero otani?
5 Amene anaperekanso chitsanzo chabwino cha khalidwe labwino anali Danieli ndi anzake achihebri atatu, otchedwa Hananiya, Misayeli, ndi Azariya. Anawatenga mokakamiza kudziko lawo ndi kumka nawo kundende ku Babulo. Anyamata anayiwo anawapatsa maina achibabulo—Belitsazara, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Anawapatsa “chakudya cha mfumu,” kuphatikizapo zakudya zoletsedwa ndi Chilamulo cha Mulungu. Ndiponso anawalamula kuchita maphunziro a zaka zitatu okhudza ‘mabuku ndi manenedwe a Akasidi.’ Zimenezi sizinali kungophunzira chinenero china basi, popeza liwu lakuti “Akasidi” panopo liyenera kuti likutanthauza anthu ophunzira. Choncho, anyamata achihebri ameneŵa anaphunzitsidwa ziphunzitso zopotoka zachibabulo.—Danieli 1:1-7.
6. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Danieli analondola khalidwe labwino?
6 Ngakhale panali zambiri zowakakamiza kutsatira zimene anaphunzira, Danieli ndi anzake atatu anasankha khalidwe labwino osati loipa. Danieli 1:21 amati: “Nakhala moyo Danieli mpaka chaka choyamba cha Koresi.” Inde, Danieli ‘anakhalabe moyo’ monga mtumiki wakhalidwe labwino wa Yehova kwa zaka zoposa 80—m’nthaŵiyi mafumu angapo amphamvu anakwera ndi kugwa. Anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu mosasamala kanthu za machenjera ndi ziŵembu za atsogoleri a boma oipa ndi khalidwe loipa la zakugonana lodzala m’chipembedzo chachibabulo. Danieli anapitirizabe kulondola khalidwe labwino.
7. Kodi tingaphunzirenji panjira imene Danieli ndi anzake atatu anatsatira?
7 Tingaphunzire zambiri kwa Danieli ameneyo woopa Mulungu ndi anzake. Iwo analondola khalidwe labwino nakana kuloŵerera m’chikhalidwe chachibabulo. Ngakhale anapatsidwa maina achibabulo, iwo anadziŵikabe monga atumiki a Yehova. Eetu, patapita zaka ngati 70, mfumu yachibabulo inaitana Danieli ndi dzina lake lachihebri! (Danieli 5:13) Pamoyo wake wonse wautaliwo, Danieli anakana kugonja ngakhale pankhani zazing’ono. Akali wamng’ono, “anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu.” (Danieli 1:8) Kusagonja kwa Danieli ndi anzake atatu kumeneku ndithudi kunawalimbitsa kupulumuka kuzengedwa mlandu kwa imfa ndi moyo kumene anakumana nako pambuyo pake.—Danieli, machaputala 3 ndi 6.
Kulondola Khalidwe Labwino Lerolino
8. Kodi Akristu achinyamata angakane motani kuloŵerera m’dziko la Satana?
8 Monga Danieli ndi anzake atatu, anthu a Mulungu lerolino amakana kuloŵerera m’dziko loipali la Satana. (1 Yohane 5:19) Ngati ndinu Mkristu wachinyamata, mwina mabwenzi anu amakukakamizani kwambiri kutsatira kavalidwe kawo konyanyako, kapesedwe, ndi nyimbo. Komabe, m’malo motsatira sitayelo iliyonse imene yabwera, imani nji, ndipo musadzilole ‘kufanizidwa ndi makhalidwe a pansi pano.’ (Aroma 12:2) ‘Kanani chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, kukhala ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.’ (Tito 2:11, 12) Chofunika kwambiri ndicho chiyanjo cha Yehova osati cha mabwenzi anu.—Miyambo 12:2.
9. Kodi Akristu amene ali m’zamalonda angayang’anizane ndi zitsenderezo zotani, ndipo kodi ayenera kukhala ndi khalidwe lotani?
9 Akristu achikulire nawonso amayang’anizana ndi zitsenderezo ndipo ayenera kukhala ndi khalidwe labwino. Akristu amene amachita malonda angaloŵe m’chiyeso chogwiritsira ntchito njira zokayikitsa kapena kunyalanyaza malamulo a boma ndi amsonkho. Komabe, kaya amene mumapikisana nawo m’malonda kapena anzanu apantchito achite bwanji, ‘tifuna kukhala nawo makhalidwe abwino.’ (Ahebri 13:18) Malemba amafuna kuti tikhale oona mtima ndi achilungamo kwa otilemba ntchito, antchito athu, makasitomala athu, ndi maboma adziko. (Deuteronomo 25:13-16; Mateyu 5:37; Aroma 13:1; 1 Timoteo 5:18; Tito 2:9, 10) Tiyeni tiyesenso kukhala adongosolo pamalonda athu. Mwa kusunga zolembedwa zolongosoka ndi kulemba zimene tagwirizana, tidzapeŵa kumvana molakwa nthaŵi zambiri.
Samalani!
10. Kodi nchifukwa ninji pafunika ‘kusamala’ pankhani ya nyimbo zimene timasankha?
10 Salmo 119:9 limatchula mbali inanso yokhala akhalidwe labwino pamaso pa Mulungu. Wamasalmo anaimba kuti: “Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mawu anu.” Chida china champhamvu kwambiri cha Satana ndicho nyimbo, zimene zimatha kukhudza mtima kwambiri. Mwachisoni, Akristu ena alephera ‘kusamala’ pankhani ya nyimbo, ndipo apeza kuti ayamba kukonda mitundu ina ya nyimbo yoipa kwambiri, monga rap ndi heavy metal. Ena angatsutse kuti nyimbo zimenezi sizimawawononga kapena kuti samamvetsera mawu ake. Ena amati amangosangalala ndi zoimbira zake zamphamvu kapena kumva kulira kokweza kwa gitala. Komabe, kwa Akristu si nkhani yoti kaya chinthu nchosangalatsa. Nkhaŵa yawo ndi yakuti kaya ‘chokondweretsa [“cholandirika kwa,” NW] Ambuye nchiyani.’ (Aefeso 5:10) Nthaŵi zambiri, nyimbo za heavy metal ndi rap zimachirikiza khalidwe loipa monga kutukwana, dama, ndipo ngakhale kulambira Satana—zinthu zimene ndithudi zilibe malo pakati pa anthu a Mulungu.a (Aefeso 5:3) Wamng’ono kapena wamkulu, aliyense wa ife angachite bwino kusinkhasinkha funsoli, Mwa nyimbo zimene ndimasankha, kodi ndikulondola khalidwe labwino kapena khalidwe loipa?
11. Kodi Mkristu angasamale motani pankhani ya maprogramu a pawailesi yakanema, mavidiyo, ndi mafilimu?
11 Maprogramu ambiri apawailesi yakanema, mavidiyo, ndi mafilimu amachirikiza khalidwe loipa. Malinga ndi kunena kwa wodziŵa za thanzi lamaganizo wina wotchuka, ‘kukondetsa kusanguluka, kugonana, chiwawa, umbombo, ndi dyera’ ndizo zadzala m’mafilimu ambiri amene akupangidwa lerolino. Choncho, kusamala kumaphatikizapo kusankha bwino zimene tikufuna kupenyerera. Wamasalmo anapemphera kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.” (Salmo 119:37) Mkristu wina wachinyamata wotchedwa Joseph anagwiritsira ntchito pulinsipulo limeneli. Pamene filimu ina inayamba kusonyeza zogonana ndi chiwawa, iye anatulukamo m’nyumba ya akanemayo. Kodi anamva manyazi pochita zimenezi? “Ayi, kutalitali,” akutero Joseph. “Ndinayamba ndaganiza za Yehova kaye ndi kuti ndimkondweretse.”
Zimene Phunziro ndi Kusinkhasinkha Zimachita
12. Kodi nchifukwa ninji phunziro laumwini ndi kusinkhasinkha nzofunika kuti tilondole khalidwe labwino?
12 Sitiyenera kungopeŵa zoipa basi. Kulondola khalidwe labwino kumaphatikizaponso kuphunzira ndi kusinkhasinkha zinthu zabwino zolembedwa m’Mawu a Mulungu kuti tigwiritsire ntchito mapulinsipulo ake olungama m’moyo. “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu,” anatero wamasalmo. “Ndilingiriramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119:97) Kodi ndandanda yanu ya mlungu ndi mlungu imaphatikizapo phunziro laumwini la Baibulo ndi phunziro la zofalitsa zachikristu? Nzoona kuti kupeza nthaŵi ya phunziro lakhama la Mawu a Mulungu ndi kusinkhasinkha mwapemphero kungakhale kovuta. Koma nthaŵi zambiri kuwombola nthaŵi kuzochita zina nkotheka. (Aefeso 5:15, 16) Mwina mmamaŵa ndi nthaŵi yabwino yoti muzipemphera, kuchita phunziro, ndi kusinkhasinkha.—Yerekezerani ndi Salmo 119:147.
13, 14. (a) Kodi nchifukwa ninji kusinkhasinkha nkofunika kwambiri? (b) Kodi tingade chisembwere mwa kusinkhasinkha malemba ati?
13 Kusinkhasinkha nkopindulitsa kwambiri, chifukwa kumatithandiza kukumbukira zimene timaphunzira. Ndipo chofunika kwambiri nchakuti kungatithandize kuchirikiza malingaliro aumulungu. Mwachitsanzo: Kudziŵa kuti Mulungu amaletsa dama nkwina ndipo ‘kudana nacho choipa ndi kugwirizana nacho chabwino’ nkwinanso. (Aroma 12:9) Tingamvedi mmene Yehova amamverera ponena za chisembwere mwa kusinkhasinkha malemba aakulu a Baibulo, monga Akolose 3:5, amene amalimbikitsa kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.” Dzifunseni kuti: ‘Kodi nchifunitso chamanyazi chotani chimene ndiyenera kufetsa? Kodi ndiyenera kupeŵanji chimene chingadzutse chilakolako chodetsedwa? Kodi pali zimene ndiyenera kusintha ndi mmene ndimachitira ndi akazi kapena amuna?’—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:1, 2.
14 Paulo akulimbikitsa Akristu kudzipatula kudama ndi kukhala odziletsa kuti “asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake.” (1 Atesalonika 4:3-7) Dzifunseni kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji kuchita dama nkovulaza? Kodi ndingadzivulaze motani kapena kuvulaza wina ngati ndachita tchimo limeneli? Kodi zingandikhudze motani mwauzimu, mumtima, ndi kuthupi? Bwanji za ena mumpingo amene aswa lamulo la Mulungu ndipo sanalape? Kodi zinthu zawakhalira bwanji?’ Kulabadira zimene Malemba amanena pakhalidwe limeneli kungakulitse chidani chathu ndi chimene chili choipa pamaso pa Mulungu. (Eksodo 20:14; 1 Akorinto 5:11-13; 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21; Chivumbulutso 21:8) Paulo amanena kuti wadama “sataya munthu, komatu Mulungu.” (1 Atesalonika 4:8) Kodi wotaya Atate wake wakumwamba angakhalenso Mkristu weniweni ngati!
Khalidwe Labwino ndi Mayanjano
15. Kodi mayanjano angachitenji pakulondola kwathu khalidwe labwino?
15 Chinanso chimene chingatithandize kukhala akhalidwe labwino ndicho mayanjano abwino. Wamasalmo anaimba kuti: “Ine ndine wakuyanjana nawo onse akukuopani [Yehova], ndi iwo akusamalira malangizo anu.” (Salmo 119:63) Mayanjano abwino opezeka pamisonkhano yachikristu ngofunika kwa ife. (Ahebri 10:24, 25) Ngati tidzipatula, tingayambe kumangoganiza zokonda ife eni, ndipo tingayambe khalidwe loipa mosavuta. (Miyambo 18:1) Komabe, mayanjano achikondi achikristu angalimbitse chosankha chathu chokhala akhalidwe labwino. Zoona, tiyeneranso kudzitetezera kumayanjano oipa. Tiyenera kukhala bwino ndi anansi, anzathu apantchito, ndi anzathu apasukulu. Koma ngati tikuyendadi mwanzeru, tidzapeŵa kuyandikana nawo kwambiri awo amene salondola khalidwe labwino lachikristu.—Yerekezerani ndi Akolose 4:5.
16. Kodi kugwiritsira ntchito 1 Akorinto 15:33 kungatithandize motani kulondola khalidwe labwino?
16 Paulo analemba kuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Potchula zimenezi, anali kuchenjeza okhulupirira kuti angataye chikhulupiriro chawo mwa kuyanjana ndi odzinenera kukhala Akristu amene anakana chiphunzitso cha m’Malemba cha chiukiriro. Pulinsipulo la chenjezo la Paulo limagwira ntchito pamayanjano athu ponse paŵiri mumpingo ndi kunja kwa mpingo. (1 Akorinto 15:12, 33) Komatu sitiyenera kunyalanyaza abale ndi alongo athu auzimu chifukwa chakuti sakuvomerezana ndi lingaliro lathu laumwini. (Mateyu 7:4, 5; Aroma 14:1-12) Ngakhale zili tero, pafunika kukhala tcheru ngati ena mumpingo ali ndi khalidwe lokayikitsa kapena ngati asonyeza mzimu waukali kapena wodandauladandaula. (2 Timoteo 2:20-22) Kuli bwino kuyandikana ndi awo amene ‘tingalimbikitsane nawo.’ (Aroma 1:11, 12) Zimenezi zidzatithandiza kulondola khalidwe labwino ndi kukhalabe ‘panjira ya moyo.’—Salmo 16:11.
Pitirizanibe Kulondola Khalidwe Labwino
17. Malinga ndi Numeri chaputala 25, kodi ndi tsoka lotani limene linagwera Aisrayeli, ndipo kodi tikuphunziraponji?
17 Kutangotsala pang’ono kuti Aisrayeli alande Dziko Lolonjezedwa, zikwi zambiri za iwo anasankha kulondola khalidwe loipa—ndipo anasakazidwa. (Numeri, chaputala 25) Lerolino, anthu a Yehova ali pafupi kuloŵa m’dziko latsopano lolungama. Kuloŵa mmenemo kudzakhala mwaŵi wadalitso la awo amene akupitirizabe kukana khalidwe loipa la dzikoli. Pokhala anthu opanda ungwiro, tingakhale ndi zikhoterero zoipa, koma Mulungu angatithandize kutsatira chitsogozo cholungama cha mzimu wake woyera. (Agalatiya 5:16; 1 Atesalonika 4:3, 4) Choncho tiyeni tilabadire chilimbikitso cha Yoswa kwa Israyeli chakuti: “Opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona.” (Yoswa 24:14) Kuopa mwaulemu kusakondweretsa Yehova kudzatithandiza kulondola khalidwe labwino.
18. Ponena za khalidwe loipa ndi khalidwe labwino, kodi Akristu onse ayenera kutsimikiza mtima kuti adzachitanji?
18 Ngati mtima wanu ukukhumba kukondweretsa Mulungu, ndiye kuti tsimikizani mtima kulabadira chilimbikitso cha Paulo chakuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” Nchiyani chidzachitika mukachita zimenezi? Paulo anati: “Zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.” (Afilipi 4:8, 9) Inde, mothandizidwa ndi Yehova mungakane khalidwe loipa ndi kulondola khalidwe labwino.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda, April 15, 1993, masamba 19-24, ndi nkhani zakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” mu Galamukani! ya February 8, March 8, ndi April 8, 1993, ndi December 8, 1996.
Mfundo Zopenda
◻ Kodi kulondola khalidwe labwino kumafunanji?
◻ Kodi Hezekiya, Danieli, ndi Ahebri atatu anasungabe khalidwe labwino m’mikhalidwe yotani?
◻ Kodi tingakhale motani ngati Danieli pokana machenjera a Satana?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kusamala pankhani ya zosangulutsa?
◻ Kodi phunziro, kusinkhasinkha, ndi mayanjano zimachitanji polondola khalidwe labwino?
[Chithunzi patsamba 15]
Hezekiya wachinyamatayo analondola khalidwe labwino ngakhale kuti anazingidwa ndi olambira Moleki
[Zithunzi patsamba 17]
Akristu ayenera kusamala pankhani ya zosangulutsa