15 Chotero, ndiye chifukwa chake iye ali mkhalapakati+ wa pangano latsopano kuti anthu amene aitanidwa alandire lonjezo la cholowa chamuyaya.+ Izi zatheka chifukwa cha imfa yake, imene inali ngati dipo+ lawo lowamasula ku machimo amene iwo anali nawo m’pangano lakale lija.+