-
Genesis 41:18-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndiyeno ndinaona ngʼombe 7 zonenepa ndi zooneka bwino zikutuluka mumtsinje wa Nailo, ndipo zinayamba kudya udzu wa mʼmbali mwa mtsinjewo.+ 19 Pambuyo pake ndinaonanso ngʼombe zina 7 zikutuluka mumtsinjewo. Ngʼombe zimenezi zinali zonyansa ndi zowonda. Sindinaonepo ngʼombe zonyansa ngati zimenezo mʼdziko lonse la Iguputo. 20 Ngʼombe zowonda ndi zonyansazo zinayamba kudya ngʼombe 7 zonenepa zija. 21 Koma ngakhale zinadya zinzakezo, palibe akanadziwa chifukwa ngʼombezo zimaonekabe zowonda ngati poyamba. Kenako ndinadzidzimuka.
-