-
Genesis 41:48, 49Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
48 Pa zaka 7 zimenezo, Yosefe anasonkhanitsa chakudya chonse chimene anakolola mʼdziko lonse la Iguputo nʼkuchisunga mʼmizinda. Mumzinda uliwonse, ankasunga chakudya chochokera mʼminda yozungulira mzindawo. 49 Yosefe anapitiriza kusunga tirigu, mpaka anachuluka kwambiri ngati mchenga wakunyanja moti anasiya kumuyeza chifukwa sakanathanso kumuyeza chifukwa anali wambiri.
-
-
Genesis 47:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiye Yosefe anati: “Ngati ndalama zakutherani, bweretsani ziweto zanu tidzasinthane ndi chakudya.”
-