18 Pa nthawi imene moyo wake unkachoka (chifukwa anali akumwalira), anapereka dzina kwa mwanayo lakuti Beni-oni. Koma bambo ake anamupatsa dzina lakuti Benjamini.+ 19 Choncho Rakele anamwalira, ndipo anamuika mʼmanda mʼmbali mwa njira yopita ku Efurata, komwe ndi ku Betelehemu.+