-
Genesis 43:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kenako Yuda anauza Isiraeli bambo ake kuti: “Ndiloleni ndimutenge mnyamatayu+ kuti tinyamuke tizipita kuti tikhalebe ndi moyo tisafe,+ inuyo ndi ife, limodzi ndi ana athuwa.+ 9 Moyo wa mnyamatayu ukhale mʼmanja mwanga.*+ Ngati chinachake chitamuchitikira mudzandilange. Ndikadzapanda kubwera naye ndi kumʼpereka kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu moyo wanga wonse.
-