-
Mateyu 24:37-39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Chifukwa mofanana ndi mmene masiku a Nowa analili,+ ndi mmenenso kukhalapo* kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.+ 38 Mʼmasiku amenewo Chigumula chisanafike, anthu ankadya ndi kumwa. Amuna ankakwatira ndipo akazi ankakwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchingalawa.+ 39 Anthu ananyalanyaza zimene zinkachitika mpaka Chigumula chinafika nʼkuwaseseratu onsewo.+ Zidzakhalanso choncho ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.
-