-
Genesis 6:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Koma dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona, ndipo linadzaza ndi chiwawa. 12 Mulungu anayangʼana dziko lapansi ndipo anaona kuti laipa.+ Anthu onse padziko lapansi ankachita zinthu zoipa.+
13 Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Ndaganiza zowononga anthu onse, chifukwa apangitsa kuti dziko lapansi lidzaze ndi chiwawa. Choncho ndiwawononga limodzi ndi zonse zimene zili padziko lapansi.+
-