-
Genesis 22:20-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Pambuyo pa zimenezi, uthenga unafika kwa Abulahamu wonena kuti: “Nayenso Milika waberekera mchimwene wako Nahori ana aamuna.+ 21 Mwana wake woyamba ndi Uza, ndiye pali mchimwene wake Buza komanso Kemueli bambo ake a Aramu. 22 Palinso Kesede, Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betuele.”+ 23 Betuele anabereka Rabeka.+ Ana 8 amenewa ndi amene Milika anaberekera Nahori mchimwene wake wa Abulahamu.
-