-
Genesis 30:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Potsirizira pake, Mulungu anakumbukira Rakele ndipo anamva pemphero lake nʼkumuthandiza kuti ayambe kubereka.*+ 23 Rakele anakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna. Ndiyeno iye anati: “Mulungu wachotsa kunyozeka kwanga.”+ 24 Choncho Rakele anapatsa mwanayo dzina lakuti Yosefe,*+ ndipo anati: “Yehova wandiwonjezera mwana wina wamwamuna.”
-