-
Deuteronomo 17:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani nʼkulitenga kukhala lanu ndipo mukukhalamo, ndiye inu nʼkunena kuti, ‘Tisankhe mfumu ngati mitundu ina yonse imene yatizungulira,’+ 15 mudzasankhe mfumu imene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ Mudzasankhe mfumuyo kuchokera pakati pa abale anu. Simukuloledwa kusankha mlendo amene si mʼbale wanu.
-
-
1 Mbiri 1:43-50Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
43 Mafumu amene analamulira dziko la Edomu,+ Aisiraeli* asanayambe kulamulidwa ndi mfumu ina iliyonse,+ ndi awa: Bela mwana wa Beori. Dzina la mzinda wake linali Dinihaba. 44 Bela atamwalira, Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozira,+ anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 45 Yobabi atamwalira, Husamu wa ku Temani, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 46 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdera la Mowabu, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. Dzina la mzinda wake linali Aviti. 47 Hadadi atamwalira, Samila wa ku Masereka anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 48 Samila atamwalira, Shauli wamumzinda wa Rehoboti, womwe unali mʼmbali mwa Mtsinje,* anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 49 Shauli atamwalira, Baala-hanani mwana wa Akibori anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 50 Baala-hanani atamwalira, Hadadi anayamba kulamulira mʼmalo mwake. Dzina la mzinda wake linali Pau ndipo mkazi wake dzina lake linali Mehetabele mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Mezahabu.
-