-
Ekisodo 25:23-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Mupangenso tebulo+ la mtengo wa mthethe, masentimita 90 mulitali, masentimita 45 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi mpaka mʼmwamba.+ 24 Mudzalikute ndi golide woyenga bwino, ndipo mudzapange mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo. 25 Mupange felemu kuzungulira tebulo lonse, muyezo wake masentimita 7* mulifupi mwake ndipo mupangenso mkombero wagolide pafelemulo. 26 Tebulolo mulipangire mphete 4 zagolide ndi kuziika mʼmakona ake 4 mmene muli miyendo yake 4. 27 Mphetezo zikhale pafupi ndi felemu kuti muzilowa ndodo zonyamulira tebulolo. 28 Mupangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo muzikute ndi golide. Ndodo zimenezi azinyamulira tebulolo.
-