-
Ekisodo 37:10-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndiyeno anapanga tebulo la mtengo wa mthethe+ masentimita 90 mulitali, masentimita 45 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi mpaka mʼmwamba.+ 11 Analikuta ndi golide woyenga bwino ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo. 12 Analipangiranso felemu kuzungulira tebulo lonse muyezo wake masentimita 7* mulifupi mwake ndipo anapanga mkombero wagolide pafelemulo. 13 Kuwonjezera pamenepo, analipangira mphete 4 zagolide nʼkuziika mʼmakona ake 4 mmene munali miyendo yake 4. 14 Mphetezo zinali pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa ndodo zonyamulira tebulolo. 15 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe nʼkuzikuta ndi golide. Ndodo zimenezi zinali zonyamulira tebulolo.
-