-
Yoswa 5:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za mʼdzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda zofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga. 12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene Aisiraeli anadya zokolola za mʼdzikomo. Kuyambira pamenepo, sipankakhalanso mana oti Aisiraeli azidya.+ Choncho chaka chimenechi nʼchimene iwo anayamba kudya zokolola za mʼdziko la Kanani.+
-