21 Musamadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.+ Mungapatse mlendo amene akukhala mumzinda wanu kuti adye, kapena mungathe kuigulitsa kwa mlendo chifukwa inu ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.
Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.+