Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 35:4-9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno Mose anauza gulu lonse la Aisiraeli kuti: “Yehova walamula kuti, 5 ‘Nonse mupereke zopereka kwa Yehova.+ Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa+ apereke kwa Yehova zinthu monga golide, siliva, kopa,* 6 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri ndi ubweya wa mbuzi.+ 7 Aperekenso zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe, 8 mafuta a nyale, basamu wopangira mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ 9 miyala ya onekisi ndi miyala ina yoika pa efodi+ komanso pachovala pachifuwa.+

  • 1 Mbiri 29:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Anthuwo anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, chifukwa anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wonse.+ Nayenso Mfumu Davide anasangalala kwambiri.

  • 2 Akorinto 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika,+ chifukwa Mulungu amakonda munthu amene amapereka mosangalala.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena