-
Ekisodo 37:17-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako anapanga choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino ndipo chinali chosula. Choikapo nyalecho chinali chinthu chimodzi ndipo chinali ndi tsinde, thunthu, timasamba tamʼmunsi mwa duwa, mphindi ndi maluwa.+ 18 Choikapo nyalecho chinali ndi nthambi 6. Kumbali ina kunali nthambi zitatu ndipo kumbali inayo kunalinso nthambi zitatu. 19 Panthambi za mbali imodzi, iliyonse inali ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Panthambi za mbali inayo, iliyonse inalinso ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyalecho anazipanga choncho. 20 Pathunthu la choikapo nyalecho panali timasamba 4 tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. 21 Mphindi imodzi inali pansi pa nthambi zake ziwiri zoyambirira. Mphindi ina inalinso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mphindi inanso inali pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zinali choncho ndi nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyale. 22 Choikapo nyale chonsecho kuphatikizapo mphindi ndi nthambi zake chinali chimodzi ndipo anachisula ndi golide woyenga bwino. 23 Kenako anachipangira nyale 7,+ zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. 24 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi anazipanga pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente imodzi.*
-