-
Ekisodo 25:31-39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Kenako mupange choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino. Choikapo nyalecho chikhale chinthu chimodzi chosula ndipo chikhale ndi tsinde, thunthu, nthambi, timasamba tamʼmunsi mwa duwa, mphindi ndi maluwa.+ 32 Choikapo nyalecho chikhale ndi nthambi 6. Kumbali ina kukhale nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kukhalenso nthambi zitatu. 33 Panthambi za mbali imodzi, iliyonse ikhale ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. Panthambi za mbali inayo, iliyonse ikhalenso ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyalecho zikhale zotero. 34 Pathunthu la choikapo nyalecho pakhale timasamba 4 tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. 35 Mphindi imodzi ikhale pansi pa nthambi zake ziwiri zoyambirira. Mphindi ina ikhalenso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mphindi inanso ikhale pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zikhale choncho ndi nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyale. 36 Choikapo nyale chonsecho, kuphatikizapo mphindi ndi nthambi zake, chikhale chimodzi ndipo chisulidwe ndi golide woyenga bwino.+ 37 Muchipangire nyale 7 ndipo nyalezo zikayatsidwa ziziunikira malo amene ali patsogolo pake.+ 38 Zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale, zikhale zagolide woyenga bwino.+ 39 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi azipange pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente imodzi.*
-