-
Ekisodo 30:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Komanso Aroni akamayatsa nyalezo madzulo, aziwotcha zofukizazo. Zimenezi ndi zofukiza zoyenera kuperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mʼmibadwo yanu yonse.
-
-
Levitiko 24:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Lamula Aisiraeli kuti akubweretsere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 3 Aroni azikhazika nyale kunja kwa katani ya Malo Oyera Koposa mʼchihema chokumanako. Nyalezo ziziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka mʼmawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale mʼmibadwo yanu yonse.
-
-
2 Mbiri 13:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo akupereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼmawa uliwonse+ ndi madzulo alionse limodzi ndi mafuta onunkhira.+ Ndipo mikate yosanjikiza*+ ili patebulo la golide woyenga bwino. Komanso madzulo alionse+ amayatsa nyale zomwe zili pachoikapo nyale chagolide.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.
-