Ekisodo 25:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Muchipangire nyale 7 ndipo nyalezo zikayatsidwa ziziunikira malo amene ali patsogolo pake.+ Ekisodo 40:24, 25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Anaika choikapo nyale+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa tebulo, kumbali yakumʼmwera ya chihemacho. 25 Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. Levitiko 24:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Lamula Aisiraeli kuti akubweretsere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+
24 Anaika choikapo nyale+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa tebulo, kumbali yakumʼmwera ya chihemacho. 25 Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
2 “Lamula Aisiraeli kuti akubweretsere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+