-
Ekisodo 28:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 “Pakati pa Aisiraeli, usankhe Aroni+ mʼbale wako pamodzi ndi ana ake+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara komanso Itamara+ kuti atumikire monga ansembe anga. 2 Aroni mʼbale wako umupangire zovala zopatulika kuti zimupatse ulemerero ndi kumʼkongoletsa.+ 3 Ulankhule ndi anthu onse aluso* amene ndinawapatsa mzimu wa nzeru.+ Anthuwo amupangire Aroni zovala zomwe zizisonyeza kuti wayeretsedwa, kuti atumikire monga wansembe wanga.
-