Ekisodo 25:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo nʼkulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikirocho.+ Ndidzakuuza malamulo onse oti ukauze Aisiraeli kuchokera pakati pa akerubi awiriwo, amene ali pamwamba pa likasa la Umboni. Levitiko 1:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 1 Yehova anaitana Mose kuchokera mʼchihema chokumanako,+ nʼkumuuza kuti: Numeri 17:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndodozo uziike mʼchihema chokumanako, patsogolo pa Umboni,+ pamene ndimakumana nawe nthawi zonse.+
22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo nʼkulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikirocho.+ Ndidzakuuza malamulo onse oti ukauze Aisiraeli kuchokera pakati pa akerubi awiriwo, amene ali pamwamba pa likasa la Umboni.