Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 30:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Guwalo uliike kutsogolo kwa katani imene ili pafupi ndi likasa la Umboni.+ Likhale patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa Umboni, pomwe ndidzaonekera kwa iwe.+

  • Levitiko 16:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni mʼbale wako kuti asamalowe mʼmalo oyera+ kuseri kwa katani,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, pa nthawi iliyonse imene wafuna, kuopera kuti angafe+ chifukwa ine ndidzaonekera mumtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+

  • Numeri 7:89
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 89 Nthawi zonse Mose akalowa mʼchihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu,+ ankamva mawu akulankhula naye kuchokera pachivundikiro+ chimene chinali pamwamba pa likasa la Umboni, pakati pa akerubi+ awiri. Mulungu ankalankhula naye mwa njira imeneyi.

  • Oweruza 20:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Kenako amuna a Isiraeli anafunsa kwa Yehova,+ chifukwa masiku amenewo likasa la pangano la Mulungu woona linali ku Beteli komweko.

  • Salimo 80:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 80 Inu Mʼbusa wa Isiraeli, mvetserani,

      Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+

      Inu amene mwakhala pampando wachifumu pamwamba* pa akerubi,+

      Onetsani kuwala kwanu.*

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena