-
Numeri 16:39, 40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Choncho wansembe Eleazara anatenga zofukizira zakopa zimene anthu amene anapsa ndi moto aja anabweretsa, ndipo anazisula nʼkupanga timalata tokutira guwa lansembe, 40 mogwirizana ndi zimene Yehova anamuuza kudzera mwa Mose. Timalatato tinali chikumbutso kwa Aisiraeli kuti munthu wamba* amene si mbadwa ya Aroni asayandikire kwa Yehova kuti akapereke nsembe zofukiza.+ Anachita zimenezi kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi anthu amene ankamutsatira anachita.+
-
-
1 Samueli 2:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ndiyeno munthu wa Mulungu anapita kwa Eli nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kodi ine sindinachititse kuti anthu amʼnyumba ya bambo ako andidziwe pamene anali akapolo kunyumba ya Farao ku Iguputo?+ 28 Pa mafuko onse a Isiraeli ndinasankha kholo lako+ kukhala wansembe wanga, kuti azipita paguwa langa lansembe+ kukapereka nsembe zanyama, azipereka nsembe zofukiza ndiponso kuti azivala efodi pamaso panga. Komanso ndinapatsa nyumba ya kholo lako nsembe zonse zotentha ndi moto za Aisiraeli.+
-