7 Aroni+ aziwotcha zofukiza zonunkhira+ kuti paguwapo+ pazikhala utsi mʼmawa uliwonse akamasamalira nyale.+ 8 Komanso Aroni akamayatsa nyalezo madzulo, aziwotcha zofukizazo. Zimenezi ndi zofukiza zoyenera kuperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mʼmibadwo yanu yonse.