37 Musapange zofukiza zanuzanu pogwiritsa ntchito zinthu zopangira zofukiza zimenezi.+ Muziona kuti zofukiza zimenezi nʼzopatulika kwa Yehova. 38 Aliyense wopanga zofukiza zofanana ndi zimenezi pofuna kusangalala ndi kafungo kake, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.”