-
Ekisodo 19:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Anthuwo uwaikire malire kuzungulira phiri lonse nʼkuwauza kuti, ‘Samalani kuti musakwere mʼphiri kapena kukhudza mʼmunsi mwake. Aliyense wokhudza phirili adzaphedwa ndithu. 13 Munthu aliyense asadzakhudze wolakwayo, koma adzaponyedwe miyala kapena kulasidwa.* Kaya ndi nyama kapena munthu, adzaphedwa.’+ Koma lipenga la nyanga ya nkhosa likadzalira,+ anthu onse adzayandikire phirilo.”
-