-
Yuda 14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ngakhalenso Inoki,+ wa mʼbadwo wa 7 kuchokera kwa Adamu, analosera za iwowa pamene anati: “Taonani! Yehova* anabwera ndi angelo ake masauzandemasauzande+ 15 kudzaweruza anthu onse,+ ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha zinthu zonyoza Mulungu zimene anachita, komanso chifukwa cha zinthu zonse zoipa kwambiri zimene ochimwa osaopa Mulunguwa anamunenera.”+
-