8 Lamba woluka*+ womangira efodi, wolumikiza ku efodiyo akhale wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Akhale wopangidwa ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.
5 Kenako utenge zovala+ zija nʼkuveka Aroni. Umuveke mkanjo ndi malaya odula manja a mkati mwa efodi. Umuvekenso efodi ndi chovala pachifuwa komanso umumange lamba* woluka wa efodi mʼchiuno mwake.+
20 Ndiyeno anapanga mphete zina ziwiri zagolide nʼkuziika kutsogolo kwa efodi, mʼmunsi mwa nsalu ziwiri zamʼmapewa, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa malo amene lamba* woluka walumikizana ndi efodi.