5 Koma iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+
Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+
Analandira chilango kuti ife tikhale pamtendere,+
Ndipo chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa.+
6 Tonsefe tikungoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa zosochera.+
Aliyense akulowera njira yake
Ndipo Yehova wachititsa kuti zolakwa za tonsefe zigwere pa ameneyo.+