Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa, azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ kuti zikhale nsembe zakupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+

  • Levitiko 5:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Koma ngati sangakwanitse kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ kuti ukhale nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lake. Asauthire mafuta ndipo asaikemo lubani chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo.

  • Levitiko 12:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi izikhala ya nsembe yopsereza, inayo izikhala ya nsembe yamachimo. Akatero wansembe adzamuphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera.’”

  • Levitiko 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma ngati munthuyo ali wosauka ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi, azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi monga nsembe yakupalamula. Nsembeyo aziiyendetsa uku ndi uku kuti amuphimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake yambewu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena