-
Levitiko 25:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ukamagula malo kwa mnzako, uziwerenga zaka zimene zadutsa kuchokera mʼChaka cha Ufulu. Azikugulitsa malowo mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kuti udzalepo mbewu.+ 16 Ngati patsala zaka zambiri, angathe kukweza mtengo wogulitsira malowo, koma ngati patsala zaka zochepa, azitsitsa mtengo wa malowo, chifukwa akukugulitsa kuchuluka kwa mbewu zimene udzakolole.
-