Levitiko 1:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ngati akupereka ngʼombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako. Levitiko 22:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Isakhale yakhungu, yothyoka fupa, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo* kapena zipere. Musamapereke kwa Yehova nyama zoterezi kapena kuwotcha nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova. Deuteronomo 15:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Koma ngati nyamayo ili ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, musamaipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.+ Deuteronomo 17:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Musamapereke kwa Yehova Mulungu wanu nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa idzakhala yonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+
3 Ngati akupereka ngʼombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako.
22 Isakhale yakhungu, yothyoka fupa, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo* kapena zipere. Musamapereke kwa Yehova nyama zoterezi kapena kuwotcha nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova.
21 Koma ngati nyamayo ili ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, musamaipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.+
17 “Musamapereke kwa Yehova Mulungu wanu nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa idzakhala yonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+