-
Numeri 25:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Pa nthawi imene Aisiraeli ankakhala ku Sitimu,+ anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.+ 2 Akaziwo anaitana Aisiraeliwo kuti azikapereka nsembe kwa milungu yawo+ ndipo Aisiraeliwo anayamba kudya nsembezo komanso kugwadira milungu ya Amowabu.+ 3 Choncho Aisiraeli anayamba kulambira nawo Baala wa ku Peori,+ ndipo Yehova anakwiya kwambiri ndi Aisiraeliwo.
-
-
Numeri 25:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 “Akhaulitseni Amidiyani ndipo muwaphe,+ 18 chifukwa akubweretserani tsoka mochenjera pokukopani kuti muchimwe ku Peori.+ Muwaphe ndithu, chifukwanso cha zochita za mchemwali wawo Kozibi, mwana wa mtsogoleri wa ku Midiyani, amene anaphedwa+ pa tsiku limene mliri unakugwerani chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”+
-