15Gawo limene linaperekedwa+ ku fuko la Yuda kuti ligawidwe kwa mabanja awo linkafika kumalire a Edomu+ ndi kuchipululu cha Zini, mpaka kumapeto kwa Negebu, kumʼmwera.
16Gawo limene ana a Yosefe+ anapatsidwa+ linayambira kumtsinje wa Yorodano kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi akumʼmawa kwa Yeriko, kudutsa kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+