15 Gawo limene linaperekedwa+ ku fuko la Yuda kuti ligawidwe kwa mabanja awo linkafika kumalire a Edomu+ ndi kuchipululu cha Zini, mpaka kumapeto kwa Negebu, kumʼmwera. 2 Malire awo akumʼmwera ankayambira kumapeto kwa Nyanja Yamchere,+ kugombe lake lakumʼmwera.